Mutu 3
Akulu adzoza ansembe ndi aphunzitsi mwa kusanjika manja. M’dzaka za pafupifupi 401–421 Yesu Atabadwa.
1 Njira imene ophunzira, amene ankatchedwa akulu a mpingo, adadzodzera ansembe ndi aphunzitsi—
2 Atatha kupemphera kwa Atate m’dzina la Khristu, adasanjika manja awo pa iwo, nati:
3 M’dzina la Yesu Khristu ndikukudzoza iwe kukhala wansembe (kapena ngati ali mphunzitsi, ndikukudzoza iwe kukhala mphunzitsi) kukalalikira kulapa ndi kuchotsedwa kwa machimo kudzera mwa Yesu Khristu, mwa chipiliro cha chikhulupiliro pa dzina lake ku chimaliziro. Ameni.
4 Ndipo mu njira yotereyi iwo adadzoza ansembe ndi aphunzitsi, molingana ndi mphatso ndi mayitanidwe a Mulungu kwa anthu; ndipo iwo adawadzoza iwo kudzera mu mphamvu ya Mzimu Woyera, umene udali mwa iwo.