Mutu 1Lehi alosera za dziko la ufulu—Mbewu yake idzabalalikana ndi kukanthidwa ngati idzakana Oyera wa Israeli—Alimbikitsa ana ake aamuna kuvala chida cha chilungamo. M’dzaka za pafupifupi 588–570 Yesu Asadabadwe. Mutu 2Chiwombolo chimabwera kudzera mwa Mesiya Oyera—Ufulu wa kudzisankhira (Upangiri) ndi ofunika mu kukhalapo ndi kupita patsogolo—Adamu adagwa kuti anthu akhale—Anthu ali omasuka kusankha ufulu ndi moyo wamuyaya. M’dzaka za pafupifupi 588–570 Yesu Asadabadwe. Mutu 3Yosefe ku Igupto adaona Anefi m’masomphenya—Iye adalosera za Joseph Smith, mlosi wa m’masiku otsiriza; za Mose, amene adzapulumutse Israeli; ndi za kubwera kwa Buku la Mormoni. M’dzaka za pafupifupi 588–570 Yesu Asadabadwe. Mutu 4Lehi alangiza ndi kudalitsa mbumba yake—Amwalira ndipo ayikidwa m’manda—Nefi alemekeza mu ubwino wa Mulungu—Nefi aika chidaliro chake mwa Ambuye kosatha. M’dzaka za pafupifupi 588–570 Yesu Asadabadwe. Mutu 5Anefi adzisiyanitsa okha kwa aLamani, asunga malamulo a Mose, ndi kumanga kachisi—Chifukwa cha kusakhulupilira kwawo, Alamani achotsedwa pamaso pa Ambuye, atembeleredwa, ndipo akhala chikwapu kwa Anefi. M’dzaka za pafupifupi 588–559 Yesu Asadabadwe. Mutu 6Yakobo alongosola za mbiri ya Ayuda: Ukapolo wa ku Babulo ndi kubwelera kwawo; utumiki ndi kupachikidwa pa mtanda kwa Oyera wa Israeli; thandizo lolandiridwa kuchokera kwa amitundu; kubwenzeretsedwa kwa Ayuda pamene adzakhulupilira mwa Mesiya m’masiku-otsiriza. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 7Yakobo apitiriza kuwerenga kuchokera mu Yesaya: Yesaya ayankhula mwa umesiya—Mesiya adzakhala ndi lilime la ophunzira—Adzapereka msana wake kwa omenya—Iye sadzasokonezedwa—Fananitsani Yesaya 50. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 8Yakobo apitiriza kuwerenga kuchokera ku Yesaya: M’masiku otsiriza, Ambuye adzatonthoza Ziyoni ndi kusonkhanitsa Israeli—Owomboledwa adzabwera ku Ziyoni pakati pa chisangalalo chachikulu—Fananitsani Yesaya 51 ndi 52:1–2. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 9Yakobo afotokoza kuti Ayuda adzasonkhanitsidwa mu m’maiko awo onse a lonjezano—Chitetezero chimawombola munthu ku kugwa—Matupi a okufa adzatuluka m’manda, ndipo mizimu yawo kuchokera ku gahena ndi ku paradiso—Iwo adzaweruzidwa—Chitetezero chimapulumutsa ku imfa, gahena, mdyerekezi, ndi mazunzo osatha—Olungama adzapulumuka mu ufumu wa Mulungu—Zilango za uchimo zikhazikitsidwa—Oyera wa Israeli ndiye mlonda wa chipata. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 10Yakobo afotokoza kuti Ayuda adzampachika Mulungu wawo—Adzamwazikana kufikira atayamba kum’khulupilira iye—Amerika adzakhala dziko la ufulu limene palibe mfumu idzalamulire—Dziyanjanitseni kwa Mulungu ndi kulandira chipulumutso kudzera mu chisomo chake. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 11Yakobo aona Muwomboli wake—Lamulo la Mose limaimira Khristu ndipo zimatsimikizira kuti Iye adzabwera. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 12Yesaya aona kachisi wa m’masiku otsiriza, kusonkhanitsa kwa Israeli, ndi chiweruzo cha dzaka chikwi ndi mtendere—Odzikweza ndi oipa adzatsitsidwa pa Kubwera Kwachiwiri—Fananitsani Yesaya 2. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 13Yuda ndi Yerusalemu adzalangidwa chifukwa cha kusamvera kwawo—Ambuye achondelera ndi kuweruza anthu awo—Ana aakazi a Ziyoni atembeleredwa ndi kuzunzidwa chifukwa cha chikunja chawo—Fananitsani Yesaya 3. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 14Ziyoni ndi ana ake aakazi adzawomboledwa ndi kuyeretsedwa m’tsiku la dzaka chikwi—Fananitsani Yesaya 4. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 15Munda wampesa wa Ambuye (Israeli) udzakhala bwinja, ndipo anthu Ake adzabalalikana—Matsoka adzafika pa iwo mu mkhalidwe wampatuko ndi kubalalikana—Ambuye adzakweza mbendera ndi kusonkhanitsa Israeli—Fananitsani Yesaya 5. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 16Yesaya aona Ambuye—Machimo a Yesaya akhululukidwa—Iye aitanidwa kuti akhale mneneri—Iye anenera za kukana kwa Ayuda kwa ziphunzitso za Khristu—Wotsalira adzabwelera—Fananitsani Yesaya 6. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 17Efraimu ndi Siriya amenya nkhondo ndi Yuda—Khristu adzabadwa mwa namwali—Fananitsani Yesaya 7. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 18Khristu adzakhala ngati mwala wopunthwitsa ndi thanthwe la chokhumudwitsa—Funani Ambuye, osati afiti owombedza—Tembenukirani ku chilamulo ndi ku umboni kuti mutsogoleledwe—Fananitsani Yesaya 8. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 19Yesaya ayankhula mwaumesiya—Anthu mum’dima adzaona kuwala kwakukulu—Kwa ife mwana watibadwira—Adzakhala Kalonga wa mtendere ndipo adzalamulira pa mpando wa chifumu wa Davide—Fananitsani Yesaya 9. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 20Chiwonongeko cha Siriya chikuimilira chiwonongeko cha oipa pa Kubwera Kwachiwiri—Anthu ochepa adzatsala Ambuye akadzabweranso kachiwiri—Otsalira a Yakobo adzabwelera mutsiku limenelo—Fananitsani Yesaya 10. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 21Tsinde la Jese (Khristu) lidzaweruza m’chilungamo—Chidziwitso cha Mulungu chidzakuta dziko lapansi mu dzaka chikwi—Ambuye adzakwezera mbendera ndi kusonkhanitsa Israeli—Fananitsani Yesaya 11. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 22M’masiku a dzaka chikwi anthu wonse adzatamanda Ambuye—Iye adzakhala pakati pawo—Fananitsani Yesaya 12. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 23Chiwonongeko cha Babulo chikuimilira chiwonongeko pa Kubwera Kwachiwiri—Lidzakhala tsiku la mkwiyo ndi kubwenzera—Babulo (dziko lapansi) adzagwa kwa muyaya—Fananitsani Yesaya 13. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 24Israeli adzasonkhanitsidwa ndipo adzasangalala ndi mpumulo wa dzaka chikwi—Lusifara adaponyedwa kuchokera kumwamba chifukwa cha kuukira—Israeli adzapambana kwa Babulo (dziko lapansi)—Fananitsani Yesaya 14. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 25Nefi alemekeza m’zomveka—Maulosi a Yesaya adzamveka bwino m’masiku otsiriza—Ayuda adzabwelera ku Babulo, adzapachika Mesiya, ndipo adzamwazikana ndi kukwapulidwa—Adzabwenzeretsedwa pamene adzakhulupilira mwa Mesiya—Iye adzabwera koyamba m’dzaka mazana asanu ndi chimodzi Lehi atachoka ku Yerusalemu—Anefi asunga lamulo la Mose ndipo akhulupilira mwa Khristu, amene ali Oyera wa Israeli. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 26Khristu adzatumikira kwa Anefi—Nefi aoneratu za chiwonongeko cha anthu ake—Iwo adzayankhula kuchokera ku fumbi—Amitundu adzamanga mipingo yonama ndi magulu azachinsinsi—Ambuye aletsa kupanga zaunsembe zolakwika. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 27Mdima ndi mpatuko zidzaphimba dziko lapansi m’masiku otsiriza—Buku la Mormoni lidzabwera—Mboni zitatu zidzachitira umboni za bukulo—Munthu ophunzira adzati sangawerenge buku lomatidwa—Ambuye adzachita ntchito yabwino ndi yodabwitsa—Fananitsani Yesaya 29. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 28Mipingo yonama yambiri idzamangidwa m’masiku omaliza—Idzaphunzitsa ziphunzitso zabodza, zopanda pake, ndi zopusa—Mpatuko udzachuluka chifukwa cha aphunzitsi abodza—Mdyerekezi adzakwiya m’mitima ya anthu—Adzaphunzitsa mitundu yonse ya ziphunzitso zabodza. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 29Amitundu ambiri adzakana Buku la Mormoni—Iwo adzati, Sitikufuna Baibulo lina—Ambuye amayankhula ku maiko ambiri—Iye adzaweruza dziko lapansi kuchokera m’ma buku amene adzalembedwa. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 30Amitundu otembenuka adzawerengedwa ndi anthu apangano—Alamani ndi Ayuda ambiri adzakhulupilira mawu ndi kukhala okondweretsa—Israeli adzabwenzeretsedwa ndipo oipa adzawonongedwa. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 31Nefi anena chifukwa chimene Khristu adabatizidwira—Anthu akuyenera kutsatira Khristu, kubatizidwa, kulandira Mzimu Woyera, ndi kupilira kufikira chimaliziro kuti apulumutsidwe—Kulapa ndi ubatizo ndi chipata cha njira yolunjika ndi yopapatiza—Moyo wamuyaya umabwera kwa iwo amene amasunga malamulo atabatizidwa. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 32Angelo amayankhula ndi mphamvu ya Mzimu Woyera—Anthu akuyenera kupemphera ndi kupeza chidziwitso cha iwo eni kuchokera kwa Mzimu Woyera. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe. Mutu 33Mawu a Nefi ndi oona—Akuchitira umboni za Khristu—Iwo amene amakhulupilira mwa Khristu adzakhulupilira mawu a Nefi, amene adzaime monga mboni pamaso pa bwalo la chiweruzo. M’dzaka za pafupifupi 559–545 Yesu Asadabadwe.