Mutu 14
Yesaya ayankhula mwaumesiya—Kunyozedwa kwa Mesiya ndi zowawa zikhazikitsidwa—Iye apanga moyo Wake kukhala nsembe ya uchimo ndi kupanga chipembedzero cha olakwa—Fananitsani Yesaya 53. M’dzaka za pafupifupi 148 Yesu Asadabadwe.
1 Inde, ngakhale Yesaya sakunena kuti: Ndani wakhulupilira mbiri yathu, ndipo mkono wa Ambuye wavumbulutsidwa kwa yani?
2 Pakuti adzaphuka pamaso pake ngati mphukira; ndi monga muzu m’nthaka youma; alibe maonekedwe kapena kukongola; ndipo pamene tidzamuona palibe kukongola kuti timukhumbire.
3 Iye adanyozedwa ndi kukanidwa ndi anthu; munthu wazisoni, ndi omvetsetsa zowawa; ndipo zidali ngati kuti tidabisa nkhope zathu kwa iye; iye adanyozedwa, ndipo ife sitidamulemekeze iye.
4 Zoonadi iye adanyamula zowawa zathu, nanyamula zisoni zathu; komabe ife tidamuyesa omenyedwa, okanthidwa ndi Mulungu, ndi osautsidwa.
5 Koma iye adalasidwa chifukwa cha zolakwa zathu, iye adavulazidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilango cha mtendere wathu chidali pa Iye; ndipo ndi mabala ake ife tachiritsidwa.
6 Ife tonse, ngati nkhosa, tasochera; tapambuka yense m’njira ya mwini yekha; ndipo Ambuye adaika pa Iye mphulupulu za ife tonse.
7 Iye adaponderezedwa, ndipo adazunzidwa, koma sadatsegule pakamwa pake; watengedwa ngati mwana wa nkhosa wopita kukaphedwa, ndi ngati mwana wankhosa ali wosayankhula pamaso pa omsenga wake, momwemo sadatsegula pakamwa pake.
8 Iye adachotsedwa ku ndende ndi ku chiweruzo; ndipo ndani adzaufotokozera za m’badwo wake? Pakuti adachotsedwa m’dziko la amoyo; chifukwa cha zolakwa za anthu anga adamenyedwa.
9 Ndipo adaika manda ake pamodzi ndi oipa, ndi olemera mu imfa yake; chifukwa sadachite choipa, ndipo m’kamwa mwake mudalibe chinyengo.
10 Koma kudakomera Ambuye kuvulaza iye; iye wamuika mu chisoni; pamene mudzapereka moyo wake nsembe ya uchimo, iye adzaona mbewu yake, adzatalikitsa masiku ake, ndipo chomkondweretsa Ambuye chidzakula m’dzanja lake.
11 Iye adzaona zowawa za moyo wake, ndikudzakhutitsidwa; ndi kudziwa kwake mtumiki wanga wolungama adzalungamitsa ambiri; pakuti adzasenza mphulupulu zawo.
12 Kotero ndidzamugawira gawo limodzi ndi akulu; ndipo adzagawa zofunkha pamodzi ndi amphamvu; chifukwa adathira moyo wake kuimfa; ndipo adawerengedwa pamodzi ndi olakwa; ndipo adanyamula machimo a ambiri, ndikupembedzera olakwa.