Yesu Khristu

Pemphero la Mgonero

  • Contents

  • Kudalitsa Mkate

  • Kudalitsa Madzi

Pemphero la Mgonero


Pemphero la Mgonero

  • Kudalitsa Mkate

    O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndikuyeretsa mkate uwu, kwa miyoyo yonse imene idye mkatewu, kuti adye pokumbukira thupi la mwana wanu, ndikuchitira umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti ndiwofunitsitsa kutenga dzina la mwana wanu, ndikum’kumbukira iye nthawi zonse ndikusunga malamulo amene anapereka kwa iwo; kuti akhale ndi Mzimu wake nthawi zonse. Amen.


  • Kudalitsa Madzi

    O Mulungu, Atate Wamuyaya, tikukupemphani mu dzina la mwana wanu, Yesu Khristu, kuti mudalitse ndikuyeretsa madzi awa, kwa miyoyo yonse imene imwe madziwa, kuti achite ichi pokumbukira mwazi wa mwana wanu, womwe unakhetsedwa mmalo mwa iwo; kuti achitire umboni kwa inu, O Mulungu, Atate Wamuyaya, kuti azimukumbukira iye nthawi zonse, kuti akhale ndi Mzimu wake. Amen.