Zofunikira Zoyambirira
Chilengezo cha Kubwezeretsa


Chibwezeretso cha Uthenga wabwino Wonse wa Yesu Khristu

Chilengezo ku Dziko lapansi cha Mazana awiri

Chilengezo ichi chidawerengedwa ndi Mtsogoleri Russell M. Nelson ngati mbali imodzi ya uthenga wake pa Msokhano 190 waukulu wapachaka pa 5 Epulo, 2020, ku Salt Lake City, Utah.

Tikulengeza motsimikiza kuti Mulungu amakonda ana Ake mu maiko onse pa dziko lapansi. Mulungu Atate watipatsa ife kubadwa kwa umulungu, moyo wosayelekezeka, ndi msembe yachipulumutso yopanda malire ya Mwana Wake Okondedwa, Yesu Khristu. Ndi mphamvu ya Atate, Yesu adaukanso ndi kupindura chigonjetso pa imfa. Iye ndi Mpulumutsi wathu, Chitsanzo chathu, ndi Muomboli wathu.

Zaka mazana awiri zapitazo, mmawa wa tsiku lokongola la m’nyengo ya masika mu 1820, m’nyamata Joseph Smith, pofuna kudziwa za mpingo oti alowe, adapita mthengo kukapemphera moyandikana kunyumba kwake mu dera la New York, USA. Adali ndi mafunso okhudzana ndi chipulumutso cha moyo wake ndipo adakhulupilira kuti Mulungu amutsogolera iye.

Modzichepetsa, tikulengeza kuti poyankha pemphero lake, Mulungu Atate ndi Mwana Wake, Yesu Khristu, adaonenekera kwa Joseph ndi kutsegulira “chibwezeretso cha zinthu zonse” (Machitidwe 3:21) monga momwe Baibulo lidaloserera. Mu masomphenya ake, iye adaphunzira kuti kutsatira imfa za Atumwi oyamba, Mpingo wa Chipangano Chatsopano wa Khristu udasowa pa dziko lapansi. Joseph adzakhala wothandiza pa kuubwenzeretsa.

Ife tikutsimikiza kuti motsogozedwa ndi Atate ndi Mwana, amithenga akumwamba adabwera kudzaphunzitsa Joseph ndi kukhazikitsanzo Mpingo wa Yesu Khristu. Yohane Mbatizi oukitsidwa adabwenzeretsa ulamuliro wobatiza pomizitsa kuti machimo akhululukidwe. Atatu mwa Atumwi khumi ndi awiri oyamba—Peturo, Yakobo, ndi Yohane—adabwezeretsa upositoli ndi mfungulo za ulamuliro wa unsembe. Enanso adabwera, kuphatikizapo Eliya, amene adabwenzera ulamuliro womanga mabanja kwamuyaya mu ubale wamoyo osatha kuposera pa imfa.

Timaperekanso umboni kuti Joseph Smith adapatsidwa mphatso ndi mphamvu ya Mulungu kuti amasulire uthenga wakale: Buku la Morimoni—Chipangano china cha Yesu Khristu. Masamba amalemba opatulikawa akuphatikizaponso nkhani yokhudza utumiki wa Yesu Khristu mwini pakati pa anthu Okhala kumadzulo atangoukitsidwa kumene. Limaphunzitsa za cholinga cha moyo ndi kulongosola chiphunzitso cha Khristu, chimene ndi thunthu la cholinga. Monga lemba lothandizana ndi Baibulo, Buku la Morimoni likuchitira umboni kuti anthu onse ndi ana aamuna ndi aakazi a Atate achikondi Akumwamba, kuti ali ndi dongosolo la umulungu pa moyo wathu, ndi kuti Mwana Wake, Yesu Khristu, amayankhulanso lero ngati m’masiku akale.

Ife tikulengeza kuti Mpingo wa Yesu Khristu wa Woyera Mtima a M’masiku Otsiriza, Okhazikitsigwa pa Epulo 6, 1830, ndi Mpingo wa Chipangano Chatsopano wa Khristu wobwenzeretsedwa. Mpingo uwu, wakhazikika pa ngodya za moyo wamngwiro wa Yesu Khristu, ndipo mu Chiyanjanitso chake chopanda malire ndi kuuka kwathunthu. Yesu Khristu waitananso Atumwi ndikuwapatsa ulamuliro wa unsembe. Iye akuyitana ife tonse kuti tibwere kwa iye ndi Mpingo Wake, kuti tidzalandire Mzimu Woyera, miyambo ya chipulumutso ndi kupeza chimwemwe chosatha.

Zaka mazana awiri zatha tsopano kuchokera pamene chibwenzeretso chimenechi chidayambika ndi Mulungu Atate ndi mwana Wake okondedwa Yesu Khristu. Zikwi za wanthu mu dziko lonse lapansi adakumbatira n’kuzindikira zochitika m’mauneneri amenewa.

Ife mokondwera tikulengeza kuti malonjezo a chibwezeretso akupitilira kudzera mu mabvumbulutso opitilira. Dziko lapansi silidzakhalanso chimodzimodzi, chifukwa Mulungu “adzasonkhanitsa pamodzi zinthu zonse mwa Khristu” (Aefeso 1:10).

Mwa ulemu ndi kuthokoza, ife monga Atumwi ake tikukuitanani nonse kuti mudziwe—ngati ife tidziwira—kuti kumwamba nkotsekula. Tikutsimikiza kuti Mulungu akudziwitsa chifuniro Chake kwa ana Ake okondedwa aamuna ndi aakazi. Ife tikuchitira umboni kuti iwo amene awerenga mwapemphero uthenga wa Chibwenzeretso ndi kuchita mwa chikhulupiliro adzadalitsidwa ndikudzapeza umboni wawo wa chi mulungu ndi cholinga chake chokonzekeretsa dziko lapansi pa lonjezo la kubweranso kwachiwiri kwa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.